...Loading...

Full Story:

Home / NATIONAL / SHOCKING: Katundu Wakwera Mtengo Mwankachibisira

236 Total Views

SHOCKING: Katundu Wakwera Mtengo Mwankachibisira

Published by Revolver Junior on 25 March 2021.

Anthu mmadera atutumuka ndikukwera mtengo kwa katundu wosiyanasiyana mwankachibisira.

Izi zachitika patangotha masiku angapo boma litalengeza za kukwera kwamafuta agalimoto (Diesel and Petro).

Motsogozana ndi kukwera mtengo kwa transport, Bulediso naye anakwera kuchokera pamtengo wa K470 kufika pa mtengo wa K57O ndipo mafuta ophikira amene amagulitsidwa pa mtengo wa K300 mu botolo la kota lita pano likugulitsidwa pa mtengo wa K400.

Titayankhula ndi Mayi wina amene amachokera ku Mbayani mu boma la Blantyre, Mayiyu anadandaula kwambiri ponena kuti zinthu zikudula kwambiri.

“Achimwene ndisakunamizeni katundu wadula, pakadalipano Mkaka wa Kerrygold, Buledi, Ufa wa Tiligu, Shuga komanso Sopo zakwerakwera mtengo, ndipo pano moyo sukuphweka monga unalili kale,” anadandaula motero Mayiyo.

Malingana ndi Mayiyo, Mkaka wa Kerrygold, Buledi, Ufa wa Tiligu, Shuga komanso Sopo ndi zinthu zimene zadziwika mwachangu kuti zakwera mtengo.


GO BACK